DAN KUMWENDA NDI WA ULERE – Malawi-Sports.com – Clubs, Football,Baseball,Basketball,Soccer,Hockey,Tennis and societies in Malawi

DAN KUMWENDA NDI WA ULERE

DAN KUMWENDA NDI WA ULERE
Share Button

Osewera wakale wa Azam Tigers yemwe anapita ku timu ya Be forward Wanderers Dan Kumwenda tsopano ndi mfulu ndipo atha kupita timu iliyonse mwa ulere atathetsa ubale wake ndi Nyerere.

Kumwenda anathesa contract yake ndi Wanderers pamodzi ndi Micheck Botomani komanso Peter Cholopi kumayambiliro a mwezi wa July.

Timu ya Wanderers inayitanisa osewerawa ndi agent wawo koma pakutha pa zokambirana zawo ndi ndalama za Botomani ndi Cholopi zomwe zaperekedwa ndipo Kumwenda wauzidwa kuti atha kusaka timu ina.

Anyamatawa anathetsa ma contract awo kamba koti timuyi imakanika kupereka ndalama zawo za ma contract.

Share Button